Romans 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga bwanji tsono? Kodi ife Ayuda tikuposa anthu a mitundu ina? Mpang'ono pomwe. Tafotokoza kale kuti onse ndi ochimwa, Ayuda ndi anthu a mitundu ina omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi timalize bwanji? Kodi Ayuda ndife oposa anthu ena? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ife tinanena kale kuti Ayuda ndi a mitundu ina omwe ndi ochimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ciani tsono? kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa agwidwa ndi ucimo;