Romans 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abrahamu ndi zidzukulu zake adalandira kwa Mulungu lonjezo lakuti dziko lapansi lidzakhala lao. Adalandira lonjezolo osati chifukwa cha kusunga Malamulo, koma chifukwa cha chilungamo chofumira m'chikhulupiriro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abrahamu ndi zidzukulu zake sanalandire lonjezano lakuti adzalandira dziko lapansi kudzera mu Malamulo, koma kudzera mu chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowanyumba wa dziko lapansi silinapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace mwa Lamulo, koma mwa cilungamo ca cikhulupiriro.