Romans 4:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adati, “Zidzukulu zako zidzachulukadi.” Ndipo ngakhale zimenezi zinali zosayembekezeka konse, Abrahamu adalimbikirabe kukhulupirira kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale zinali zosayembekezeka, Abrahamu anakhulupirira ndi chiyembekezo kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri. Izi ndi monga zinanenedwa kwa iye kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amene anakhulupira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa conenedwaci, Mbeu yakoidzakhala yotere,