Romans 4:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zaka zake zinali pafupi makumi khumi, ndipo adaadziŵa kuti thupi lake linali ngati lakufa kale, ndiponso kuti Sara anali wouma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye osafooka m'chikhulupiriro sanalabadira thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanafowoke mʼchikhulupiriro. Anadziwa choonadi cha thupi lake kuti linali lakufa popeza anali ndi zaka pafupifupi 100 ndiponso mimba ya Sara inali yowuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye osafoka m'cikhulupiriro sanalabadira thupi lace, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;