Romans 5:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati, pokhala ife adani ace, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wace, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wace.