Romans 5:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho monga momwe tchimo linalowa mʼdziko lapansi kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mu tchimo, mʼnjirayi imfa inafika kwa anthu onse pakuti onse anachimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, monga ucimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa ucimo; cotero imfa inafikira anthu onse, cifukwa kuti onse anacimwa.