Romans 5:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu imfa inachita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanachimwa monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe, imfa inalamulira kuyambira nthawi ya Adamu mpaka nthawi ya Mose. Inalamulira ngakhalenso pa iwo amene sanachimwe posamvera Malamulo monga anachitira Adamu. Adamuyo amene anali chifaniziro cha wina amene ankabwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu imfa inacita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanacimwa monga macimwidwe ace a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo.