Romans 5:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mphatso siinadza monga mwa mmodzi wakuchimwa, pakuti mlandu ndithu unachokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere ichokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso, mphatso ya Mulungu sifanana ndi zotsatira za kuchimwa kwa munthu mmodzi. Chiweruzo chinatsatira tchimo la munthu mmodzi ndi kubweretsa kutsutsidwa koma mphatso inatsatira zolakwa zambiri ndi kubweretsa kulungamitsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mphatso siinadza monga mwa mmodzi wakucimwa, pakuti mlandu ndithu unacokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere icokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.