Romans 5:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ngati, chifukwa cha kulakwa kwa munthu mmodziyo, imfa inalamulira kudzera mwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga kwa iwo amene adzalandira chisomo chochuluka ndi mphatso yachilungamo, adzalamulira mʼmoyo kudzera mwa munthu mmodzi, Yesu Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inacita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kucuruka kwace kwa cisomo ndi kwa mphatso ya cilungamo, adzacita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Kristu.