Romans 5:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho monga tchimo limodzi linabweretsa kutsutsika pa anthu onse, chimodzimodzinso ntchito imodzi yolungama inabweretsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuwapatsa moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; comweconso mwa cilungamitso cimodzi cilungamo ca moyo cinafikira anthu onse.