Romans 5:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malamulo a Mulungu anaperekedwa ndi cholinga chakuti anthu onse azindikire kuchuluka kwa machimo awo. Koma pamene machimo anachuluka, chisomo chinachuluka koposa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo lamulo linalowa moyenjezera, kuti kulakwa kukacuruke; koma rl pamene ucimo unacuruka, pomwepo cisomo cinacuruka koposa;