Romans 5:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.