Romans 6:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo musapereke ziwalo zanu kuucimo, zikhale zida za cosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo ataturuka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za cilungamo,