Romans 6:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bwanji tsono? Kodi tizichimwabe popeza kuti chimene chimalamulira moyo wathu si Malamulo, koma kukoma mtima kwa Mulungu? Iyai, mpang'ono pomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ciani tsono? Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri a lamulo, koma a cisomo? Msatero ai.