Romans 6:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kucilungamo?