Romans 6:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuucimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli naco cobala canu cakufikira ciyeretso, ndi cimariziro cace moyo wosatha.