Romans 6:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tinaikldwa m'manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.