Romans 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi tsono ndiye kuti chinthu chabwinochi chidandiphetsa? Mpang'ono pomwe. Koma uchimo ndiwo udandipha pakugwiritsa ntchito chinthu chabwinocho kuti khalidwe lenileni la uchimowo liwonekere poyera kuti ndi uchimodi. Motero kudzera mwa malamulo, uchimo umaoneka woipa kopitirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano chabwino chija chinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma uchimo, kuti uoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa ndithu mwa lamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi chomwe ndi chabwino tsopano chinasanduka imfa kwa ine? Si choncho ayi! Koma kuti uchimo uzindikirike kuti ndi uchimo unabala imfa mwa ine kudzera mu chomwe chinali chabwino, kotero kuti kudzera mu lamulo uchimo ukhale oyipa kopitirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano cabwino cija cinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma ucimo, kuti uoneke kuti uli ucimo, wandicitira imfa mwa cabwino cija; kuti ucimo ukakhale wocimwitsa ndithu mwa lamulo.