Romans 7:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindimvetsa bwino zimene ndimachita. Pakuti sindichita zimene ndifuna kuchita, koma zomwe ndimadana nazo, nzimene ine ndimazichita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine sindizindikira zimene ndimachita. Pakuti zimene ndimafuna kuchita sindizichita koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimazichita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cimene ndicita sindicidziwa; pakuti sindicita cimene ndifuna, koma cimene ndidana naco, ndicita ici.