Romans 7:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikudziŵa kuti mwa ine simukhala kanthu kabwino. Ndikamati, “ine”, ndikunena khalidwe langa lokonda zoipa. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, komabe sindizichita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikudziwa kuti mwa ine mulibe kanthu kabwino, ndiye kuti mʼthupi langa lauchimo. Pakuti ndimafuna kuchita zabwino, koma ndimalephera kuzichita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala cinthu cabwino; pakuti kufuna ndiri nako, koma kucita cabwino sindikupeza.