Romans 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwachitsanzo, Malamulo amati mkazi wokwatiwa ndi womangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wakeyo nthawi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma ngati mwamuna wake amwalira, mkaziyo ndi womasulidwa ku lamulo la ukwati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wace wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.