Romans 7:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ndimaona kuti chimene chimachitika nchakuti pamene ndifuna kuchita zabwino, zoipa zili nane pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ndapeza kuti lamuloli likugwira ntchito. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, zoyipa zili nane pomwepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cotero odipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna cabwino, coipa ciriko.