Romans 7:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m'ziwalo zanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mʼkati mwanga ndimaona lamulo lina likugwira ntchito kulimbana ndi zomwe mtima wanga umavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa wamʼndende walamulo la uchimo lomwe likugwira ntchito mʼkati mwa ziwalo zanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m'ziwalo zanga.