Romans 7:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ngati adzipereka kwa mwamuna wina, pamene mwamuna wake ali moyo, mkaziyo amati ngwachigololo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi uja wamasuka ku malamulo a ukwati, kotero kuti sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina pamene mwamuna wake ali moyo, amatchedwa wachigololo. Koma ngati mwamuna wakeyo amwalira, mkaziyo amasuka ku lamulo ndipo si wachigololo, ngakhale kuti wakwatiwa ndi mwamuna wina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cifukwa cace, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wace wamoyo, adzanenedwa mkazi wacigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; cotero sakhala wacigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.