Romans 7:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene tinkatsata mkhalidwe wathu wachibadwa, zilakolako zoipa zimene Malamulo adaaziwutsa zinkagwira ntchito mwa ife, ndipo zidabala imfa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti pamene tinkalamulidwa ndi khalidwe lathu lauchimo, zilakolako zauchimo zimene Malamulo anaziwutsa zinkagwira ntchito mʼmatupi mwathu kotero kuti zinabala imfa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za macimo, zimene zinali mwa cilamulo, zinalikucita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso,