Romans 7:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano tamasuka ku Malamulowo. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi Malamulo amene kale ankatimanga. Tsopano Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mwa njira yatsopano, osatinso mwa njira yakale ija yakungotsata Malamulo olembedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsopano tinamasulidwa kuchilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'chilembo chakale ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsopano tinamasulidwa kucilamulo, popeza tinafa kwa ici cimene tinagwidwa naco kale; cotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'cilembo cakale ai.