Romans 8:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.