Romans 8:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikudziŵa kuti mpaka tsopano zolengedwa zonse zakhala zikubuula ndi kumva zoŵaŵa, zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tikudziwa kuti chilengedwe chonse chakhala chikubuwula ndi ululu ngati ululu wa nthawi yobereka mwana mpaka tsopano lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tidziwa kuti colengedwa conse cibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.