Romans 8:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde, Mulungu adatipulumutsa, koma tikuyembekezabe chipulumutsocho. Koma tsono tikamaona ndi maso zimene tikuziyembekezazi, apo si chiyembekezonso ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ife tinapulumutsidwa mʼchiyembekezo ichi. Koma chiyembekezo chimene chimaoneka si chiyembekezo ayi. Kodi ndani amene amayembekezera chimene ali nacho kale?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ife tinapolumutsidwa ndi ciyembekezo; koma ciyembekezo cimene cioneka si ciri ciyembekezo ai; pa kuti ayembekezera ndani cimene acipenya?