Romans 8:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo iye amene asanthula m'mitima adziwa cimene acisamalira Mzimu, cifukwa apempherera oyera mtima monga mwa cifuno ca Mulungu.