Romans 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale anawo asanabadwe, ndiye kuti tsono asanachite chilichonse chabwino kapena choipa, Mulungu adaafunabe kuti cholinga chake chosankhira munthu aliyense chipitirire. Izi adachita osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifukwa chakuti Mulungu adamuitana munthuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo,