Romans 9:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungunso ndi momwemo. Adaafuna kuwonetsa mkwiyo wake, nafunanso kuti mphamvu zake zidziŵike. Komabe adapirira moleza mtima kwambiri zochita za anthu amene Iye adaaŵakwiyira, ndipo amene adaayeneradi kuwonongedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuonetsa mkwiyo wace, ndi kudziwitsa mph amvu yace, analekerera ndi cilekerero cambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera cionongeko?