Romans 9:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi monga momwe Mulungu akunenera m'buku la mneneri Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga, ndidzaŵatcha ‘Anthu anga’. Mtundu umene sindinkaukonda, ndidzautcha ‘Wokondedwa wanga’.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawatcha anthu anga; ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawacha anthu anga; Ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.