Romans 9:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mneneri Yesaya adaanena mokweza mau za Aisraele kuti, “Ngakhale Aisraele achuluke ngati mchenga wakunyanja, koma oŵerengeka okha adzapulumuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti, “Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiye adzapulumuke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yesaya apfuula za Israyeli, kuti, 2 Ungakhale unyinji wa ana a Israyeli ukhala monga mcenga wa kunyanja, 3 cotsalira ndico cidzapulumuka.