Romans 9:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikadakonda kuti m'malo mwao, ineineyo ndikhale wotembereredwa, osakhalanso wake wa Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndikadafunakuti ine ndekha nditembereredwe kundicotsa kwa Kristu cifukwa ca abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;