Romans 9:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani? Chifukwa ankafuna kupezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, osati pakukhulupirira, koma pakudalira ntchito zabwino. Adaphunthwa pa mwala wophunthwitsa anthu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chanji? Chifukwa kuti sanachitsata ndi chikhulupiriro, koma monga ngati ndi ntchito. Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa canji? Cifukwa kuti sanacitsata ndi cikhulupiriro, koma monga ngati ndi nchito. 7 Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa;