Romans 9:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa ndi zidzukulu za makolo athu akale aja, ndipo Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi wa mtundu wao, kunena za umunthu wake. Mulungu amene amalamulira zonse, alemekezeke mpaka muyaya. Amen.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anacokera Kristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka ku nthawi zonse. Amen.