Ruth 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bwererani ana anga, muzipita kwanu, pakuti ndakalamba kwambiri, sindingathenso kukhala ndi mwamuna. Ngakhale ndikadanena kuti chikhulupiriro chilipobe, ngakhale ndikadakhala ndi mwamuna usiku uno, kuti ndibale ana aamuna,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindikhoza kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana amuna;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bwererani kwanu ana anga muzipita kwanu. Ine ndakalamba kwambiri kotero kuti sindingakwatiwenso. Ngakhale ndikananena kuti ndili nacho chikhulupiriro, ngakhale ndikanakhala ndi mwamuna usiku uno, ndipo nʼkubala ana aamuna,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindikhoza kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndiri naco ciyembekezo, ndikakhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana amuna;