Ruth 1:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Naomi adauza Rute kuti, “Ona, mbale wako wabwerera kwao ndi kwa milungu yake. Nawenso bwerera, umulondole mbale wakoyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wake, bwerera umtsate mbale wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Naomi anati “Taona, mʼbale wako wabwerera kwawo kwa anthu ake ndi kwa milungu yake. Bwerera nawenso umulondole mʼbale wako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wace, bwerera umtsate mbale wako.