Ruth 1:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Rute adamuuza kuti, “Musandiwumirize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndisakutsateni. Kumene mupite inuko, inenso ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inuko, inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Rute anayankha kuti, “Musandikakamize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndibwerere osakutsatani. Kumene inu mupite ine ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika