Ruth 1:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho aŵiriwo adapitirira ulendo wao, mpaka adakafika ku Betelehemu. Akaziwo atafika ku Betelehemuko, anthu onse am'mudzimo adatekeseka chifukwa cha iwowo. Tsono akazi ena ankati, “Kodi ameneyu ndi Naomi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho amayi awiriwo anapitiriza ulendo wawo mpaka anakafika ku Betelehemu. Pamene ankafika mu Betelehemu, anthu onse a mʼmudzimo anatekeseka chifukwa cha iwowo ndipo amayi ambiri ankanena kuti, “Kodi uyu nʼkukhala Naomi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?