Ruth 1:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo anali Elimeleki, mkazi wake anali Naomi. Ana ake aŵiriwo anali Maloni ndi Kiliyoni. Onsewo anali Aefurati a ku Betelehemu m'dziko la Yuda, koma adapita ku Mowabu nakhala komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzina la munthuyo linali Elimeleki, dzina la mkazi wake linali Naomi, ndipo mayina a ana awo aamuna anali Maaloni ndi Kiliyoni. Iwo anali Aefurati ochokera ku Betelehemu ku Yuda. Ndipo anapita kukakhala ku Mowabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wace ndiye Naomi, ndi maina a ana ace awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo a ku Efrata ku Betelelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Moabu, nakhala komweko.