Ruth 1:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaapita ndili ndi zinthu zambiri, koma Chauta wandibweza ndili wopanda kanthu. Motero munditchulirenji Naomi pamene Mphambe wandisautsa ndi kundigwetsera mavuto oŵaŵa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinapita wolemera, koma Yehova wabwera nane wopanda kanthu. Nanga munditchulirenji Naomi pamene Yehova wandisautsa. Wamphamvuzonse uja wandigwetsera mavuto owawa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinacoka pane wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; mundicheranji Naomi, popeza Yehova wandicitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandicitira cowawa?