Ruth 1:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umu ndi m'mene Naomi adabwerera kuchokera ku Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake wachimowabu uja. Ndipo adafika ku Betelehemu pa nthaŵi yoyamba kudula barele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Naomi anabwerera kuchoka ku dziko la Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake. Ndipo anafika ku Betelehemu nthawi yoyamba kukolola barele.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmoabu mpongozi wace pamodzi naye, amene anabwera kucokera ku dziko la Moabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kuceka barele.