Ruth 1:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa adakwatira akazi achimowabu. Wina dzina lake anali Olipa, winayo anali Rute. Adakhala ku Mowabuko pafupi zaka khumi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anakwatira akazi a Chimowabu; wina dzina lake Oripa ndi wina Rute. Atakhala kumeneko pafupifupi zaka khumi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadzitengera iwo akazi a ku Moabu; wina dzina lace ndiye Olipa, mnzace dzina lace ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.