Ruth 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mkaziyo ndi apongozi ake aŵiri aja adayamba kukonza ulendo wobwerera kwao kuchokera ku Mowabu, poti anali atamva ku Mowabuko kuti Chauta adadalitsa anthu ake ndi kuŵapatsa chakudya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Naomi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kubwerera kwawo kuchokera ku Mowabu popeza anali atamva ali ku Mowabuko kuti Yehova anakomera mtima anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ace kuti abwerere kucoka m'dziko la Moabu; pakuti adamva m'dziko la Moabu kuti Yehova adasamalira anthu ace ndi kuwapatsa cakudya.