Ruth 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Naomi adauza apongozi ake aŵiri aja kuti, “Pitani, aliyense abwerere kwa mai wake. Chauta akuchitireni zabwino, monga momwe mudachitira malemu aja ndi ine ndemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, “Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Naomi anati kwa apongozi ace awiri, Mukani, bwererani yense wa inu ku nyumba ya amai wace; Yehova akucitireni zokoma, monga umo munacitira akufa aja ndi ine.