Ruth 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuthandizeni kuti mupeze pokhala, ndipo aliyense mwa inu akwatiwe.” Pompo adaŵampsompsona. Koma iwo adayamba kulira mokweza,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova akuthandizeni kuti aliyense wa inu apeze pokhala pabwino komanso mwamuna.” Kenaka anawapsompsona koma awiriwo analira mokweza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wace. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.