Ruth 2:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Bowazi adayankha kuti, “Zonse zimene wakhala ukuchitira mpongozi wako, kuyambira nthaŵi imene mwamuna wako adamwalira, ndazimva zonsezo. Ndamvanso kuti udasiya bambo wako, mai wako ndi dziko lako, ndipo wabwera kwa anthu amene sudaŵadziŵe ndi kale lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bowazi anayankha kuti, “Ine ndawuzidwa zonse zimene wakhala ukuchitira apongozi ako chimwalirire mwamuna wako. Ndamvanso kuti unasiya abambo ndi amayi ako komanso dziko la kwanu ndi kubwera kudzakhala ndi anthu amene sumawadziwa ndi kale lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Boazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unacitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi mako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.