Ruth 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Rute adati, “Mwandikomera mtima kwambiri mbuyanga, mwandisangalatsa ndipo mwandilankhula mwachifundo, ngakhale sindine mmodzi mwa adzakazi anu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rute anati, “Mwandikomera mtima, mbuye wanga. Ndipo mwandisangalatsa ndi kundiyankhula mwa chifundo ngakhale sindili mmodzi mwa adzakazi anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena cokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.